Joshua 9:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adavala nsapato zothaitha za zigamba zokhazokha, ndiponso zovala zansanza. Buledi amene adatenga anali wouma ndi wachuku.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi nsapato zakale za zigamba pa mapazi ao, nizivala nsanza; ndi mikate yonse ya kamba wao inali youma ndi yoyanga nkhungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthuwa anavala nsapato zakutha ndi zazigamba ndiponso anavala sanza. Buledi wawo yense anali wowuma ndi wowola.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi nsapato zakale za zigamba pa mapazi ao, nizibvala nsanza; ndi mikate yonse ya kamba wao inali youma ndi yoyanga nkhungu.