Jude 1:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma anthu ameneŵa amachita chipongwe zinthu zimene sazidziŵa. Ndipo zinthu zimene amazidziŵa ndi nzeru zachibadwa, zonga za nyama, ndizo zimene zimaŵaononga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma iwowa zimene sazidziwa azichitira mwano; ndipo zimene azizindikira chibadwire, monga zamoyo zopanda nzeru, mu izi atayika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma anthu awa amachita chipongwe zinthu zimene sakuzidziwa. Ndipo zinthu zimene amazidziwa ndi nzeru zachibadwa, monga za nyama, ndizo zimene zimawawononga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma iwowa zimene sazidziwa azicitira mwano; ndipo zimene azizindikira cibadwire, monga zamoyo zopanda nzeru, mu izi atayika,