Jude 1:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwoŵa ali ndi tsoka, chifukwa adatsata njira ya Kaini. Monga adaachitira Balamu, iwonso adagwa m'cholakwa chifukwa chotsata phindu la ndalama. Adaonongeka chifukwa cha kuukira Mulungu, monga adaachitira Kora.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsoka kwa iwo! Pakuti anayenda m'njira ya Kaini, ndipo anadziononga m'chisokero cha Balamu chifukwa cha kulipira, natayika m'chitsutsano cha Kora.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsoka kwa iwo chifukwa anatsatira njira ya Kaini. Iwo athamangira phindu, nʼchifukwa chake anagwa mʼtchimo la Baalamu. Iwo anawonongedwa chifukwa chowukira monga anachitira Kora.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsoka kwa iwo! pakuti anayenda m'njira ya Kaini, ndipo anadziononga m'cisokero ca Balamu cifukwa ca kulipira, natayika m'citsutsano ca Kore,