Jude 1:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ameneŵa ndiwo amaipitsa maphwando anu achikondi. Amadya nanu mochitisa manyazi, nangosamala za iwo okha. Ali ngati mitambo youluzika ndi mphepo, koma osadzetsa mvula. Ali ngati mitengo yosabala zipatso ngakhale pa nyengo yake, imene idaferatu ndipo anthu adaizula.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iwo ndiwo okhala mawanga pa maphwando anu a chikondano, pakudya nanu pamodzi, akudziweta okha opanda mantha; mitambo yopanda madzi, yotengekatengeka ndi mphepo; mitengo ya masika yopanda zipatso, yofafa kawiri, yozuka mizu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu amenewa ndiwo amayipitsa maphwando anu achikondi. Amadya nanu mopanda manyazi ndipo ali ngati abusa amene amangodzidyetsa okha. Anthuwa ali ngati mitambo yowuluzika ndi mphepo, yopanda mvula. Ali ngati mitengo ya nthawi ya masika, yopanda zipatso, yozuka mizu, mitengo yoferatu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iwo ndiwo okhala mawanga pa mapwando anu a cikondano, pakudya nanu pamodzi, akudziweta okha opanda mantha; mitambo yopanda madzi, yotengekatengeka ndi mphepo; mitengo ya masika yopanda zipatso, yofafa kawid, yozuka mizu;