Jude 1:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
kuti adzaweruze anthu onse. Adzagamula kuti ngolakwa onse osasamala za Mulungu, chifukwa cha ntchito zao zonse zosalungama, zimene adachita mosaopa Mulungu. Adzaŵatsutsa chifukwa cha mau onse achipongwe amene iwo, anthu ochimwa ndi onyozera za Mulungu, adanyoza nawo Ambuye.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kudzachitira onse chiweruziro, ndi kutsutsa osapembedza onse, pa ntchito zao zonse zosapembedza, ndi pa zolimba zimene ochimwa osapembedza adalankhula pa Iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
kuti adzaweruze aliyense, ndi kudzagamula kuti onse osapembedza ndi olakwa, chifukwa cha ntchito zawo zosalungama zimene anachita mʼmoyo wawo osaopa Mulungu. Adzawatsutsa chifukwa cha mawu onse achipongwe amene osapembedzawa ananyoza nawo Ambuye.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kudzacitira onse ciweruziro, ndi kutsutsa osapembedza onse, pa nchito zao zonse zosapembedza, zimene anazicita kosapembedza, ndi pa zolimba zimene ocimwa osapembedza adalankhula pa iye.