Jude 1:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu ake ndi aŵa: ong'ung'udza, odandaula, ndi omangotsata zilakolako zao zoipa. Amalankhula zonyada, ndipo amangotamanda anthu moshashalika chifukwa chofuna kupezerapo phindu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Amenewo ndiwo odandaula, oderera, akuyenda monga mwa zilakolako zao (ndipo pakamwa pao alankhula zazikuluzikulu), akutama anthu chifukwa cha kupindula nako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu amenewa amangʼungʼudza ndi kudandaula. Amatsatira zilakolako zawo zoyipa. Amayankhula zodzitamandira ndipo amanamiza ena pofuna kupeza phindu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Amenewo ndiwo odandaula, oderera, akuyenda monga mwa zilakolako zao (ndipo pakamwa pao alankhula zazikuruzikuru), akutama anthu cifukwa ca kupindula nako.