Jude 1:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma ena muŵapulumutse pakuŵalanditsa ku moto. Enanso muŵachitire chifundo, koma mwamantha, muzidana ngakhale ndi chovala chao chomwe choipitsidwa ndi machimo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma ena muwapulumutse ndi kuwakwatula kumoto; koma ena muwachitire chifundo ndi mantha, nimudane naonso malaya ochitidwa mawanga ndi thupi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ena muwapulumutse powalanditsa ku moto. Enanso muwachitire chifundo, koma mwa mantha, ndipo muzidana ngakhale ndi mwinjiro yomwe yayipitsidwa ndi machimo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma ena 6 muwapulumutse ndi kuwakwatula kumoto; koma ena muwacitire cifundo ndi mantha, 7 nimudane naonso maraya ocitidwa mawanga ndi thupi