Jude 1:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mukumbukire angelo amene sadakhutire ndi ulamuliro wao, koma adasiya malo amene Mulungu adaaŵapatsa. Mulungu adaŵamanga ndi maunyolo osatha, ndipo akuŵasunga m'malo amdima mpaka tsiku lalikulu lija pamene adzaŵaweruza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Angelonso amene sanasunga chikhalidwe chao choyamba, komatu anasiya pokhala paopao, adawasunga m'ndende zosatha pansi pa mdima, kufikira chiweruziro cha tsiku lalikulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo mukumbukire angelo amene sanakhutire ndi maudindo awo, koma anasiya malo awo. Angelo amenewa Mulungu anawamanga ndi maunyolo osatha, ndipo akuwasunga mʼmalo a mdima mpaka tsiku lalikulu lachiweruzo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Angelonso amene sanasunga cikhalidwe cao coyamba, komatu anasiya pokhala pao pao, adawasunga m'ndende zosatha pansi pa mdima, kufikira ciweruziro ca tsiku lalikuru.