Jude 1:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mukumbukirenso mizinda ya Sodomu ndi Gomora ija, ndi mizinda yoyandikana nayo. Anthu ake m'menemonso ankangochita dama, namachitanso zonyansa zotsutsana ndi umunthu. Mulungu adaaŵaika ngati chitsanzo pakuŵalanga ndi moto wosatha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Monga Sodomu ndi Gomora, ndi midzi yakuizungulira, potsatana nayoyo, idadzipereka kudama, ndi kutsata zilakolako zachilendo, iikidwa chitsanzo, pakuchitidwa chilango cha moto wosatha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Musayiwale mizinda ya Sodomu ndi Gomora ija, ndi mizinda yoyandikana nayo. Anthu mʼmenemo anadziperekanso kuchita zadama ndi kuchita zonyansa zachilendo. Mizinda imeneyi yakhala ngati chitsanzo cha amene adzalangidwa ndi moto wosatha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Monga; Sodoma ndi Gomora, ndi midzi yakuizungulira, potsatana nayoyo, idadzipereka kudama, ndi kursara zilakolako zacilendo, iikidwa citsanzo, pakucitidwa cilango ca mota wosatha.