Jude 1:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma ngakhale Mikaele yemwe, mkulu wa angelo, pamene iye ankakangana ndi Satana ndi kutsutsana naye za mtembo wa Mose, sadafune kutchuliliza mwachipongwe kuti ndi wolakwa. Adangoti, “Ambuye akulange!”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Mikaele mkulu wa angelo, pakuchita makani ndi mdierekezi anatsutsana za thupi la Mose, sanalimbika mtima kumtchulira chifukwa chomchitira mwano, koma anati, Ambuye akudzudzule.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ngakhale mkulu wa angelo Mikayeli, pamene ankalimbana ndi Mdierekezi za mtembo wa Mose, sanamunene kuti wachipongwe, koma anati, “Ambuye akudzudzule iwe!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Mikayeli mkulu wa angelo, pakucita makani ndi mdierekezi anatsutsana za thupi la Mose, sanalimbika mtima kumehulira cifukwa comcitira mwano, koma anati, Ambuye akudzudzule.