Judges 1:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Kalebe adati, “Mkulu wa ankhondo amene athire nkhondo mzinda wa Kiriyati-Sefere, naulanda, ndidzampatsa mwana wanga Akisa kuti akhale mkazi wake.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Kalebe anati, Iye amene akantha mudzi wa Kiriyati-Sefere, naulanda, yemweyo ndidzampatsa Akisa mwana wanga wamkazi akhale mkazi wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Kalebe anati, “Munthu amene angathire nkhondo mzinda wa Kiriati Seferi ndi kuwulanda, ndidzamupatsa mwana wanga Akisa kuti akhale mkazi wake.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Kalebe anati, iye amene akantha mudzi wa Seferi, naulanda, yemweyo ndidzampatsa Akisa mwana wanga wamkazi akhale mkazi wace.