Judges 1:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iye adayankha kuti, “Ndimati mundipatseko mphatso. Popeza kuti mwandikhazika m'dziko la Negebu lopanda madzi, mundipatsenso akasupe a madzi.” Pamenepo Kalebe adampatsa akasupe akumtunda ndi akuchigwa omwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati kwa iye, Mundipatse dalitso; popeza mwandipatsa dziko la kumwera, ndipatsenso zitsime za madzi. Pamenepo Kalebe anampatsa zitsime za kumtunda ndi zitsime za kunsi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anayankha kuti, “Mundikomere mtima. Popeza mwandipatsa ku Negevi, kumalo kumene kulibe madzi, mundipatsenso akasupe amadzi.” Choncho Kalebe anamupatsa akasupe a kumtunda ndi a kumunsi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati kwa Iye, Mundipatse dalitso; popeza mwandipatsa dziko lakumwela, ndipatsenso zitsime za madzi. Pamenepo Kalebe anampatsa zitsime za kumtunda ndi zitsime za kunsi.