Judges 1:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono zidzukulu za Mkeni uja, mpongozi wa Mose, zidapita nawo limodzi anthu a fuko la Yuda kuchokera ku mzinda wamigwalangwa mpaka ku chipululu chimene chili kumwera kwa Aradi, m'dziko la Yuda. Kumeneko adakakhala ndi Aamaleke.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ana a Mkeni mlamu wake wa Mose, anakwera kutuluka m'mudzi wa m'migwalangwa pamodzi ndi ana a Yuda, nalowa m'chipululu cha Yuda chokhala kumwera kwa Aradi; namuka iwo nakhala ndi anthuwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono zidzukulu za Hobabu, Mkeni uja, mpongozi wa Mose, zinachoka ku Yeriko mzinda wa migwalangwa pamodzi ndi anthu a fuko la Yuda mpaka ku chipululu chimene chili kummwera kwa Aradi ndi kukakhala ndi Aamaleki.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ana a Mkeni mlamu wace wa Mose, anakwera kuturuka m'mudzi wa m'migwalangwa pamodzi ndi ana a Yuda, nalowa m'cipululu ca Yuda cokhala kumwela kwa Aradi; namuka iwo nakhala ndi anthuwo.