Judges 1:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ayuda adatsakana ndi abale ao Asimeoni ndipo adagonjetsa Akanani amene ankakhala mu mzinda wa Zefati, naononga mzindawo kwathunthu. Choncho mzindawo adautcha Horima.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yuda anamuka ndi Simeoni mkulu wake, nakantha Akanani akukhala m'Zefati, nauononga konse. Koma dzina la mudziwo analitcha Horoma.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka anthu a fuko la Yuda anapita pamodzi ndi abale awo a fuko la Simeoni ndi kukagonjetsa Akanaani amene amakhala ku Zefati, ndipo mzindawo anawuwononga kwambiri. Choncho mzindawo anawutcha Horima.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yuda anamuka ndi Simeoni mkuru wace, nakantha Akanani akukhala m'Zefati, nauononga konse. Koma dzina la mudziwo analicha Horima.