Judges 1:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthuyo adapita ku dziko la Ahiti nakamangako mzinda nkuutcha dzina loti Luzi. Limenelo ndilo dzina lake mpaka pano.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo munthuyo anamuka ku dziko la Ahiti, namanga mudzi, nautcha dzina lake Luzi; ndilo dzina lake mpaka lero lino.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo iye anapita ku dziko la Ahiti, kumene anamangako mzinda nawutcha dzina lake Luzi. Mpaka lero lino mzindawo dzina lake ndi lomwelo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo munthuyo anamuka ku dziko la Ahiti, namanga mudzi, naucha dzina lace Luzi; ndilo dzina lace mpaka lero lino.