Judges 1:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma a fuko la Manase sadapirikitse nzika za mu Beteseani ndi za m'midzi yake yozungulira, kapenanso nzika za mu Taanaki ndi za m'midzi yake yozungulira. Sadapirikitsenso nzika za mu Dori ndi za m'midzi yake yozungulira, kapenanso nzika za mu Ibleamu ndi za m'midzi yake yozungulira. Nazonso nzika za mu Megido ndi za m'midzi yake yozungulira sadazipirikitse. Choncho Akanani adapitirirabe kukhala m'dzikomo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Manase sanaingitse a ku Beteseani ndi midzi yake kapena a Taanaki ndi midzi yake, kapena nzika za ku Dori ndi midzi yake, kapena nzika za ku Ibleamu ndi midzi yake, kapena nzika za ku Megido ndi midzi yake; koma Akanani anakhumba kukhala m'dziko muja.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma a fuko la Manase sanachotse nzika za mzinda wa Beti-Seani pamodzi ndi mʼmidzi yake yozungulira, kapena nzika za mzinda wa Taanaki ndi mʼmidzi yake yozungulira, kapenanso nzika za mzinda wa Dori ndi mʼmidzi yake yozungulira. Iwo sanapirikitse nzika za mzinda wa Ibuleamu ndi mʼmidzi yake yozungulira, kapena mzinda wa Megido ndi mʼmidzi yake yozungulira. Choncho Akanaani anapitirirabe kukhala mʼdzikomo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Manase sanaingitsa a ku Betiseani ndi midzi yace kapena a Taanaki ndi midzi yace, kapena nzika za ku Dori ndi midzi yace, kapena nzika za ku Ibleamu ndi midzi yace, kapena nzika za ku Megido ndi midzi yace; koma Akanani anakhumba kukhala m'dziko muja.