Judges 1:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Ayuda adauza abale ao, anthu a fuko la Simeoni, kuti, “Tiyeni tipite limodzi m'dziko limene Chauta adagaŵira ife, kuti tikamenyane ndi Akanani. Pambuyo pake nafenso tidzapita nanu limodzi m'dziko limene adagaŵira inu.” Choncho Asimeoni adatsakana nawo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yuda ananena ndi Simeoni mkulu wake, Kwera nane ku gawo langa kuti tiwathire nkhondo Akanani; ndipo inenso ndidzamuka nawe ku gawo lako. Namuka naye Simeoni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Ayuda anawuza abale awo a fuko la Simeoni kuti, “Bwerani tipitire limodzi mʼdziko limene tapatsidwa kuti tikamenyane ndi Akanaani. Ifenso tidzapita nanu mʼdziko limene anakugawirani.” Ndipo Asimeoni anapita nawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yuda ananena ndi Simeoni mkuru wace, Kwera nane ku gawo langa kuti tiwathire nkhondo Akanani; ndipo inenso ndidzamuka nawe ku gawo lako. Namuka naye Simeoni.