Judges 1:30 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Azebuloni sadapirikitse nzika za mu Kitironi ndi nzika za mu Nahaloli. Choncho Akananiwo ankakhala pakati pao nasanduka oŵagwirira ntchito yaukapolo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Zebuloni sanaingitse nzika za ku Kitironi, kapena za ku Nahaloli; koma Akanani anakhala pakati pao, nawasonkhera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Azebuloni sanathamangitse Akanaani amene amakhala mu Kitironi kapena a ku Nahaloli. Iwo ankakhala pakati pawo ndipo ankawagwiritsa ntchito yakalavulagaga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Zebuloni sanaingitsa nzika za ku Kitroni, kapena nzika za ku Nahaloli; koma Akanaru anakhala pakati pao, nawasonkhera.