Judges 1:33 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anafutali sadapirikitse nzika za mu Betesemesi ndi nzika za mu Betanati, koma ankakhala pakati pa Akananiwo, nzika za dzikolo. Komabe nzika za mu Betesemesi ndi za mu Betanati ankazigwiritsa ntchito yaukapolo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nafutali sanaingitse nzika za ku Betesemesi, kapena nzika za ku Betanati; koma anakhala pakati pa Akanani, nzika za kudziko; koma nzika za ku Betesemesi, ndi a ku Betanati zinawasonkhera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nalonso fuko la Nafutali silinathamangitse anthu amene ankakhala ku Beti Semesi kapena ku Beti Anati. Koma Anafutaliwo ankakhala pakati pa Akanaaniwo mʼdzikomo. Koma anthu amene ankakhala ku Beti Semesi ndi ku Beti Anati anawasandutsa kukhala ogwira ntchito yathangata.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nafitali sanaingitsa nzika za ku Beti-semesi, kapena nzika za ku Beri-anati; koma anakhala pakati pa Akanani, nzika za kudziko; koma nzika za ku Beti-semesi, ndi a ku Beti-anati zinawasonkhera.