Judges 1:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Adonibezeki adati, “Mafumu makumi asanu ndi aŵiri oduka zala zazikulu zakumanja ndi zakumwendo ankatola nyenyeswa pansi pa tebulo langa. Mulungu wandichita zomwe ndidaŵachita iwowo.” Anthu ake adapita naye ku Yerusalemu ndipo iye adafera komweko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anati Adoni-Bezeki, Mafumu makumi asanu ndi awiri odulidwa zala zazikulu za m'manja ndi m'mapazi anaola kakudya kao pansi pa gome panga; monga ndinachita ine, momwemo Mulungu wandibwezera. Ndipo anadza naye ku Yerusalemu, nafa iye komweko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Adoni-Bezeki anati, “Mafumu 70 omwe anadulidwa zala zazikulu za ku manja ndi miyendo yawo ankatola nyenyeswa pansi pa tebulo langa. Mulungu tsopano wandibwezera zomwe ndinawachita.” Kenaka anapita naye ku Yerusalemu ndipo anafera komweko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anati Adoni-bezeki, Mafumu makumi asanu ndi awiri odulidwa zala zazikuru za m'manja ndi m'mapazi anaola kakudya kao pansi pa gome panga; monga ndinacita ine, momwemo Mulungu wandibwezera. Ndipo anadza naye ku Yerusalemu, nafa iye komweko.