Judges 10:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atafa Abimeleki, padabwera winanso wodzapulumutsa Aisraele. Iyeyu anali Tola, mwana wa Puwa, mdzukulu wa Dodo, wa fuko la Isakara. Ankakhala ku Samiri, m'dziko lamapiri la Efuremu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atafa Abimeleki, anauka kupulumutsa Israele Tola mwana wa Puwa, mwana wa Dodo munthu wa Isakara; nakhala iye m'Samiri ku mapiri a Efuremu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atafa Abimeleki panabwera Tola mwana wa Puwa, mdzukulu wa Dodo kudzapulumutsa Aisraeli. Iyeyu anali wa fuko la Isakara ndipo ankakhala ku Samiri mʼdziko la mapiri la Efereimu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atafa Abimeleki, anauka kupulumutsa Israyeli Tola mwana wa Puwa, mwana wa Dodo munthu wa Isakara; nakhala iye m'Sanriri ku mapiri a Efraimu.