Judges 10:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pitani mukalirire milungu imene mwaisankhulayo. Ikupulumutseni milungu imeneyo pa nthaŵi ya kuzunzika kwanu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mukani ndi kufuulira kwa milungu munaisankha, ikupulumutseni nyengo ya kusauka kwanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pitani kalireni kwa milungu imene mwayisankha. Iyoyo ikupulumutseni ku mavuto anuwo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mukani ndi kupfuulira kwa milungu munaisankha, ikupulumutseni nyengo ya kusauka kwanu.