Judges 10:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Aisraele adayankha Chauta kuti, “Ai, tachimwadi ife, tichiteni zimene zikukomereni. Tapota nanu, mungotipulumutsako lero lokha.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ana a Israele anati kwa Yehova, Tachimwa, mutichitire monga mwa zonse zikomera pamaso panu; komatu mutipulumutse lero lino, tikupemphani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Aisraeli anayankha Yehova kuti, “Ife tachimwa. Tichitireni chimene mukuona kuti ndi chabwino, koma chonde tipulumutseni lero lokha.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ana a Israyeli anati kwa Yehova, Tacimwa, muticitire monga mwa zonse zikomera pamaso panu; komatu mutipulumutse lero lino, tikupemphani.