Judges 10:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono anthuwo ndi atsogoleri a Agiliyadi adayamba kufunsana kuti, “Kodi munthu woti ayambe kumenyana ndi Aamoniŵa ndani? Iyeyo ndiye amene akhale mtsogoleri wolamulira anthu onse a ku Giliyadi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anthu, akalonga a Giliyadi, ananenana wina ndi mnzake, Ndaniyo adzayamba kulimbana ndi ana a Amoni? Iye adzakhala mkulu wa onse okhala m'Giliyadi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka anthuwo ndi atsogoleri a Agiliyadi anayamba kufunsana kuti, “Kodi ndi munthu wotani amene atayambe kuthira nkhondo Aamoni? Iyeyu adzakhala mtsogoleri wolamulira anthu onse a ku Giliyadi.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anthu, akalonga a Gileadi, ananenana wina ndi mnzace, Ndaniyo adzayamba kulimbana ndi ana a Amoni? iye adzakhala mkuru wa onse okhala m'Gileadi.