Judges 10:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iyeyu anali nawo ana makumi atatu amene ankakwera pa abulu makumi atatu. Anawo anali nayonso mizinda makumi atatu imene mpaka pano ikutchedwa Havoti-Yairo m'dziko la Giliyadi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anali nao ana amuna makumi atatu okwera pa ana a abulu makumi atatu, iwo ndipo anali nayo midzi makumi atatu, otchedwa midzi ya Yairi, mpaka lero lino, ndiyo m'dziko la Giliyadi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iyeyu anali ndi ana aamuna makumi atatu, amene ankakwera pa abulu makumi atatu. Iwo anali ndi mizinda makumi atatu mʼdziko la Giliyadi, imene mpaka lero ikutchedwa kuti Havoti Yairi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anali nao ana amuna makumi atatu okwera pa ana a aburu makumi atatu, iwo ndipo anali nayo midzi makumi atatu, ochedwa midzi ya Yairi, mpaka lero lino, ndiyo m'dziko la Gileadi.