Judges 10:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aisraele adachitanso zoipira Chauta potumikira Abaala ndi Aasitaroti, milungu ya ku Siriya, milungu ya ku Sidoni, milungu ya ku Mowabu, milungu ya Aamoni ndiponso milungu ya Afilisti. Aisraelewo adasiyadi Chauta osamamtumikiranso ai.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ana a Israele anaonjeza kuchita choipa pamaso pa Yehova, natumikira Abaala, ndi Aasitaroti, ndi milungu ya Aramu, ndi milungu ya Sidoni, ndi milungu ya Mowabu, ndi milungu ya ana a Amoni, ndi milungu ya Afilisti; ndipo anamleka Yehova osamtumikira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aisraeli anachitanso zoyipira Yehova. Iwo anatumikira Abaala ndi Asitoreti, milungu ya ku Aramu, Sidoni, Mowabu, Aamoni ndi Afilisti. Choncho analeka osatumikiranso Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ana Israyeli a anaonjeza kucita coipa pamaso pa Yehova, natumikira Abaala, ndi Aastaroti, ndi milungu ya Aramu, ndi milungu ya Sidoni, ndi milungu ya Moabu, ndi milungu ya ana a Amoni, ndi milungu ya Afilisti; ndipo anamleka Yehova osamtumikira.