Judges 10:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo Aamoni adaoloka mtsinje wa Yordani kukamenyana nkhondo ndi fuko la Yuda, la Benjamini ndiponso la Efuremu, kotero kuti Aisraele adazunzika kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ana a Amoni anaoloka Yordani kuthiranso nkhondo Yuda ndi Benjamini, ndi nyumba ya Efuremu; napsinjika kwambiri Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aamori anawoloka mtsinje wa Yorodani kukathira nkhondo mafuko a Yuda, Benjamini ndi Efereimu kotero kuti Israeli anavutika kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ana a Amoni anaoloka Yordano kuthiranso nkhondo Yuda ndi Benjamini, ndi nyumba ya Efraimu; napsinjika kwambiri Israyeli.