Judges 11:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mfumu ya Aamoniyo idaŵayankha amithenga a Yefita kuti, “Chifukwa chakuti Aisraele, pochoka ku Ejipito, adalanda dziko langa kuyambira ku mtsinje wa Arinoni mpaka ku mtsinje wa Yaboki mpakanso ku mtsinje wa Yordani. Tsono mundibwezere dziko mwamtendere.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu ya ana a Amoni inati kwa mithenga ya Yefita, Chifukwa Israele analanda dziko langa pakukwera iye kuchokera ku Ejipito, kuyambira Arinoni mpaka Yaboki, ndi mpaka Yordani; ndipo tsopano undibwezere maikowa mwamtendere.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo mfumu ya Aamoni inayankha amithenga a Yefita aja kuti, “Pamene Israeli amatuluka kuchokera mu Igupto, analanda dziko langa kuyambira ku mtsinje wa Arinoni mpaka ku mtsinje wa Yaboki mpakanso ku mtsinje wa Yorodani. Tsopano mundibwezere dziko langa mwamtendere.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu ya ana a Amoni inati kwa mithenga ya Yefita, Cifukwa Israyeli analanda dziko langa pakukwera iye kucokera ku Aigupto, kuyambira Arinoni mpaka Yaboki, ndi mpaka Yordano; ndipo tsopano uodibwezere maikowa mwamtendere.