Judges 11:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi imeneyo Aisraele adatuma amithenga kwa mfumu ya ku Edomu kukaiwuza kuti, ‘Tapota nanu, mutilole kuti tidzere m'dziko mwanu.’ Koma mfumu ya ku Edomuyo sidafune kumva zimenezo. Adatumanso amithenga ena kwa mfumu ya ku Mowabu, koma nayonso sidavomereze zimenezo. Choncho Aisraele adakhala ku Kedesi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pamenepo Israele anatuma mithenga kwa mfumu ya Edomu, ndi kuti, Ndikupemphani ndipitire pakati pa dziko lanu; koma mfumu ya Edomu siinamvera. Natumanso kwa mfumu ya Mowabu; nayenso osalola; ndipo Israele anakhala m'Kadesi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Israeli anatumiza amithenga kwa mfumu ya ku Edomu kuti, ‘Chonde tiloleni kuti tidutse mʼdziko lanu,’ Koma mfumu ya ku Edomu sinamvere zimenezo. Aisraeli anatumizanso amithenga kwa mfumu ya ku Mowabu, ndipo iyo inakananso. Choncho Israeli anakhala ku Kadesi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pamenepo Israyeli anatuma mithenga kwa mfumu ya Edomu, ndi kuti, Ndikupemphani ndipitire pakati pa dziko lanu; koma mfumu ya Edomu sinamvera. Natumanso kwa mfumu ya Moabu; nayenso osalola; ndipo Israyeli anakhala m'Kadesi.