Judges 11:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake adanyamuka ulendo wao kudzera ku chipululu nazungulira dziko la Edomu ndi dziko la Mowabu, ndipo adafika kuvuma kwa Arinoni. Koma sadaloŵe m'dziko la Mowabu, pakuti mtsinje wa Arinoni unali malire a dziko la Mowabu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anayenda m'chipululu, naphazira dziko la Edomu, ndi dziko la Mowabu, nadzera kum'mawa kwa dziko la Mowabu, namanga misasa tsidya lija la Arinoni; osalowa malire a Mowabu, pakuti Arinoni ndi malire a Mowabu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Pambuyo pake, Aisraeli ananyamuka ulendo kudzera ku chipululu nazungulira dziko la Edomu ndi dziko la Mowabu, ndipo anafika ku mmawa kwa dziko la Mowabu ndi kumanga zinthando zawo ku mbali ina ya mtsinje wa Arinoni. Iwo sanalowe mʼdziko la Mowabu, chifukwa mtsinje wa Arinoni ndiwo unali malire a dziko la Mowabu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anayenda m'cipululu, naphazira dziko la Edomu, ndi dziko la Moabu, nadzera kum'mawa kwa dziko la Moabu, namanga misasa tsidya lija la Arinoni; osalowa malire a Moabu, pakuti Arinoni ndi malire a Moabu.