Judges 11:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake Aisraele adatuma amithenga kwa Sihoni mfumu ya Aamori, amene ankalamula ku Hesiboni. Aisraelewo adamupempha kuti, ‘Tapota nanu, mutilole kuti tidzere m'dziko mwanu popita kwathu.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Israele anatuma mithenga kwa Sihoni mfumu ya Aamori, mfumu ya ku Hesiboni; nanena naye Israele, Tikupemphani tipitire pakati pa dziko lanu, kunka kwathu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Pambuyo pake Israeli anatumiza amithenga kwa Sihoni mfumu ya Aamori, amene amalamulira ku Hesiboni ndipo anati kwa iye, ‘Chonde tiloleni kuti tidutse mʼdziko lanu popita kwathu.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Israyeli anatuma mithenga kwa Sihoni mfumu ya Aamori, mfumu ya ku Hesiboni; nanena naye Israyeli, Tikupemphani tipitire pakati pa dziko lanu, kumka kwathu.