Judges 11:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Giliyadi analinso ndi mkazi amene anali ndi ana. Tsono ana amenewo atakula, adampirikitsa Yefita namuuza kuti, “Sudzalandirako choloŵa m'nyumba ya bambo wathu, pakuti ndiwe mwana wa kwa mkazi wina.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mkazi wa Giliyadi anambalira ana amuna; koma atakula ana amuna a mkaziyo anampirikitsa Yefita, nanena naye, Sudzalandira cholowa m'nyumba ya atate wako; pakuti ndiwe mwana wa mkazi wina.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mkazi wake wa Giliyadi anabereka naye ana aamuna. Tsono ana amenewa atakula anapirikitsa Yefita ndi kumuwuza kuti, “Sudzalandirako cholowa mʼnyumba ya abambo athu chifukwa ndiwe mwana wa mkazi wina.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mkazi wa Gileadi anambalira ana amuna; koma atakula ana amuna a mkaziyo anampitikitsa Yefita, nanena naye, Sudzalandira colowa m'nyumba ya atate wako; pakuti ndiwe mwana wa mkazi wina.