Judges 11:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Sihoni sadaŵalole Aisraele kuti adzere m'dziko mwake. Kenaka Sihoni adasonkhanitsa anthu ake onse, nakamanga zithando zankhondo ku Yahazi, ndipo adamenyana nkhondo ndi Aisraele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Sihoni sanakhulupirire Israele kuti apitire pakati pa malire ake; koma Sihoni anamemeza anthu ake onse, namanga misasa ku Yahazi, nathira nkhondo Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Sihoni sanalole Israeli kuti adzere mʼdziko mwake. Mʼmalo mwake Sihoni anasonkhanitsa ankhondo ake onse nakamanga msasa ku Yahazi ndipo anachita nkhondo ndi Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Sihoni sanakhulupirira Israyeli kuti apitire pakati pa malire ace; koma Sihoni anamemeza anthu ace onse, namanga misasa ku Yahazi, nathira nkhondo Israyeli.