Judges 11:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Chauta, Mulungu wa Aisraele, adampereka Sihoniyo pamodzi ndi anthu ake onse m'manja mwa Aisraele naŵagonjetsa. Choncho Aisraele adalanda chigawo chonse cha dziko la Aamori amene ankakhala m'dzikolo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova Mulungu wa Israele anapereka Sihoni ndi anthu ake onse m'dzanja la Israele, ndipo anawakantha, ndi Israele, analandira cholowa chake, dziko lonse la Aamori, nzika za m'dziko lija.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Koma Yehova Mulungu wa Israeli anamupereka Sihoni pamodzi ndi anthu ake onse mʼmanja mwa Israeli, ndipo anawagonjetsa. Choncho Aisraeli analanda dziko lonse la Aamori amene amakhala mʼdzikolo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova Mulungu wa Israyeli anapereka Sihoni ndi anthu ace onse m'dzanja la Israyeli, ndipo anawakantha, ndi Israyeli analandira colowa cace, dziko lonse la Aamori, nzika za m'dziko lija.