Judges 11:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho ndi Chauta, Mulungu wa Aisraele, amene adalandira Aisraele anthu ake maiko a Aamori. Nanga inu mukufuna kutilandanso maikowo?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Motero Yehova Mulungu wa Israele anaingitsa Aamori, pamaso pa anthu ake Israele, ndipo kodi liyenera kukhala cholowa chanu?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ndiye kuti Yehova Mulungu wa Aisraeli ndiye analanda dziko la Aamori, kuwalandirira anthu ake. Kodi inu mukufuna kutilanda dzikolo?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Motero Yehova Mulungu wa Israyeli anaingitsa Aamori, pamaso pa anthu ace Israyeli, ndipo kodi liyenera kukhala colowa canu?