Judges 11:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Khalani ndi dziko limene mulungu wanu Kemosi wakupatsani kuti likhale lanu. Koma maiko onse amene Chauta Mulungu wathu watilandira, akhala athu ndithu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chimene akulandiritsani Kemosi mulungu wanu, simuchilandira cholowa chanu kodi? Momwemo aliyense Yehova Mulungu wathu waingitsa pamaso pathu, zakezo tilandira cholowa chathu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Bwanji inu osakhazikika mʼdziko limene Kemosi mulungu wanu anakupatsani, ifenso tikhazikike mʼdziko limene Yehova Mulungu wathu anatipatsa?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cimene akulandiritsani Kemosi mulungu wanu, simucilandira colowa canu kodi? Momwemo ali yense Yehova Mulungu wathu waiogitsa pamaso pathu, zacezo tilandira colowa cathu.