Judges 11:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa zaka mazana atatu Aisraele ankakhala ku Hesiboni ndi m'milaga yake, ku Aroere ndi m'milaga yake, ndiponso m'mizinda yonse imene ili m'mbali mwa mtsinje wa Arinoni, nanga chifukwa chiyani simunkalanda malowo nthaŵi imeneyo?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pokhala Israele m'Hesiboni ndi midzi yake, ndi m'Aroere ndi midzi yake ndi m'midzi yonse yokhala m'mphepete mwa Arinoni zaka mazana atatu; munalekeranji kulandanso nthawi ija?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene Aisraeli ankakhala mʼdziko la Hesiboni ndi mʼmidzi yake, mʼdziko la Aroeri ndi midzi yake, komanso mʼmizinda yonse imene ili mʼmbali mwa mtsinje wa Arinoni kwa zaka 300, nʼchifukwa chiyani inu simunalande malowo nthawi imeneyo?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pokhala Israyeli m'Hesiboni ndi midzi yace, ndi m'Aroeri ndi midzi yace, ndi m'midzi yonse yokhala m'mphepete mwa Arinoni zaka mazana atatu; munalekeranji kulandanso nthawi ija?