Judges 11:29 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Mzimu wa Chauta udatsikira Yefita, ndipo iye adanyamuka nadzera ku Giliyadi ndi ku Manase. Adakafika ku Mizipa, mzinda wa Giliyadi, ndipo kuchokera ku Mizipako adakafika kumbuyo kwa Aamoni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo mzimu wa Yehova unamdzera Yefita, napitira iye ku Giliyadi, ndi Manase, napitira ku Mizipa wa Giliyadi, ndi kuchokera ku Mizipa wa Giliyadi anapitira kwa ana a Amoni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Mzimu wa Yehova unatsikira pa Yefita. Ndipo iye ananyamuka nadzera ku Giliyadi ndi ku Manase. Anafika ku Mizipa mʼdziko la Giliyadi, ndipo kuchokera kumeneko anapita kukalimbana ndi Aamoni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo mzimu wa Yehova unamdzera Yefita, napitira iye ku Gileadi, ndi Manase, napitira ku Mizipa wa Gileadi, ndi kucokera ku Mizipa wa Gileadi anapitira kwa ana a Amoni.