Judges 11:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho Yefita adaŵathaŵa abale akewo nakakhala m'dziko la Tobu. Kumeneko adakakopa anzake achabechabe kuti azimtsata ndi kunka nasakaza zinthu pamodzi naye.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Yefita anathawa abale ake, nakhala m'dziko la Tobu; ndipo anyamata opanda pake anasonkhana kwa Yefita, natuluka naye pamodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Yefita anathawa kuchoka kwa abale ake ndi kukakhala mʼdziko la Tobu. Kumeneko anakakopa ndi kusonkhanitsa anthu achabechabe ndipo anatuluka pamodzi kukasakaza zinthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Yefita anathawa abale ace, nakhala m'dziko la Tobu; ndipo anyamata opanda pace anasonkhana kwa Yefita, naturuka naye pamodzi.