Judges 11:33 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adaŵakanthadi kuyambira ku Aroere mpaka pafupi ndi mzinda wa Miniti, mizinda makumi aŵiri pamodzi, ndiponso mpaka ku Abele-Keranimu. Motero Aamoni adagonjetsedwa ndi Aisraele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nawakantha kuyambira ku Aroere mpaka ufika ku Miniti, ndiyo midzi makumi awiri, ndi ku Abele-Keranimu, makanthidwe akulu ndithu. Motero ana a Amoni anagonjetsedwa pamaso pa ana a Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anawononga mizinda makumi awiri kuchokera ku Ariori mpaka pafupi ndi mzinda wa Miniti. Anapitirira mpaka ku Abeli-Keranimu. Choncho Aisraeli anagonjetsa Aamoni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nawakantha kuyambira ku Aroeri mpaka ufika ku Miniti, ndiyo midzi makumi awiri, ndi ku Abelikerami, makanthidwe akuru ndithu. Motero ana a Amoni anagonjetsedwa pamaso pa ana a Israyeli.