Judges 11:34 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake Yefita adabwerera kwao ku Mizipa. Ndipo adangoona mwana wake wamkazi akutuluka kudzamchingamira, akuimba ng'oma ndi kumavina. Iye anali mwana wake mmodzi yekhayo. Analibenso mwana wina, wamwamuna kapena wamkazi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pofika Yefita ku Mizipa kunyumba yake, taonani, mwana wake wamkazi anatuluka kudzakomana naye ndi malingaka ndi kuthira mang'ombe; ndipo iyeyu anali mwana wake mmodzi yekha, analibe mwana wina wamwamuna kapena wamkazi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pambuyo pake Yefita anabwerera ku nyumba yake. Tsono anangoona mwana wake wamkazi akutuluka kudzamuchingamira akuyimba ngʼoma ndi kuvina. Uyu anali mwana yekhayo wa Yefita. Analibenso mwana wina wamwamuna kapena wamkazi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pofika Yefita ku Mizipa ku nyumba yace, taonani, mwana wace wamkazi anaturuka kudzakomana naye ndi malingaka ndi kuthira mang'ombe; ndipo iyeyu anali mwana wace mmodzi yekha, analibe mwana wina wamwamuna kapena wamkazi.