Judges 11:35 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yefita atamuwona mwana wake wamkaziyo, adang'amba zovala zake nati, “Kalanga ine, iwe mwana wanga! Wandidula mtima ndipo wandibweretsera mavuto aakulu kopambana, pakuti ndidalonjeza Chauta ndi pakamwa pangapa ndipo sindingathe kubweza malumbiro anga.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali, pakumuona anang'amba zovala zake, nati, Tsoka ine, mwana wanga, wandiweramitsa kwakukulu, ndiwe wa iwo akundisaukitsa ine; pakuti ndamtsegulira Yehova pakamwa panga ine, ndipo sinditha kubwerera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yefita ataona mwana wake uja, anangʼamba zovala zake ndi kulira, “Kalanga ine! Mwana wanga! Wandivulaza kwambiri ndipo iwe ndi gwero la mavuto anga. Ine ndinalumbira kwa Yehova ndi pakamwa pangapa ndipo sindingathe kubweza malumbiro angawo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali, pakumuona anang'amba zobvala zace, nati, Tsoka ine, mwana wanga, wandiweramitsa kwakukuru, ndiwe wa iwo akundisaukitsa ine; pakuti ndamtsegulira Yehova pakamwa panga ine, ndipo sinditha kubwerera.