Judges 11:38 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Bambo wakeyo adamuuza kuti, “Pita.” Adamulola kuti apite pa miyezi iŵiri. Choncho mtsikanayo adachoka pamodzi ndi anzake kunka ku mapiri, namakalira kuti akukafa osakwatiwa, opanda mwana.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati iye, Muka. Namuuza amuke akakhale miyezi iwiri; namuka iye ndi anzake, nalirira unamwali wake pamapiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yefita anamuyankha kuti, “Pita.” Ndipo anamulola kuti apite miyezi iwiri. Tsono anapita kumapiri ndi atsikana anzake kukalira chifukwa cha unamwali wake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati iye, Muka. Namuuza amuke akakhale miyezi iwiri; namuka iye ndi anzace, nalirira unamwali wace pamapiri.