Judges 11:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Yefita adaŵafunsa akuluakulu a ku Giliyadiwo kuti, “Kodi suja inu mudadana nane nkundipirikitsa ku nyumba ya bambo wanga? Chifukwa chiyani tsopano mwabwera kwa ine poona kuti muli m'mavuto?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yefita anati kwa akulu a Giliyadi, Simunandida kodi, ndi kundichotsa m'nyumba ya atate wanga? Ndipo mundidzeranji tsopano pokhala muli m'kusauka?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yefita anawawuza Agiliyadi kuti, “Kodi inu suja munkadana nane ndi kundithamangitsa ku nyumba ya abambo anga? Nʼchifukwa chiyani lero mwabwera kwa ine pamene muli pa mavuto?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yefita anati kwa akulu a Gileadi, Simunandida kodi, ndi kundicotsa m'nyumba ya atate wanga? ndipo mundidzeraoji tsopano pokhala muli m'kusauka?