Judges 11:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo akuluakuluwo adamuyankha Yefita kuti, “Nchimene tabwerera kwa iwe tsopano lino, kuti upite nafe kukamenyana ndi Aamoni, ndipo ukhale mtsogoleri wathu wolamulira anthu onse a ku Giliyadi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo akulu a Giliyadi ananena ndi Yefita, Chifukwa chake chakuti takubwerera tsopano ndicho kuti umuke nafe ndi kuchita nkhondo ndi ana a Amoni, nudzakhala mkulu wathu wa pa onse okhala m'Giliyadi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Akuluakulu a ku Giliyadi aja anamuyankha kuti, “Chimene tabwerera kwa iwe ndi chakuti upite nafe kukamenyana ndi Aamoni, ndipo udzakhala wolamulira wa onse okhala mu Giliyadi.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo akuru a Gileadi ananena ndi Yefita, Cifukwa cace cakuti takubwerera tsopano ndico kuti umuke nafe ndi kucita nkhondo ndi ana a Amoni, nudzakhala mkuru wathu wa pa onse okhala m'Gileadi.