Judges 12:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aefuremu adakonzeka kuti akamenye nkhondo, ndipo adaolokera ku Zafoni nakafunsa Yefita kuti, “Chifukwa chiyani udaaoloka kukamenya nkhondo ndi Aamoni, ife osatiitana kuti tipite nao? Tikutenthera m'nyumba mwakomu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo amuna a Efuremu analalikidwa, napita kumpoto; nati kwa Yefita, Wapitiriranji kuthira nkhondo ana a Amoni, osatiitana ife timuke nawe? Tidzakutenthera nyumba yako ndi moto pamtu pako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Gulu la nkhondo la fuko la Efereimu linayitanidwa ndipo anawolokera ku Zafoni nakafunsa Yefita kuti, “Nʼchifukwa chiyani unawoloka kukachita nkhondo ndi Aamoni osatiyitana kuti tipite nawe? Ife tikutenthera mʼnyumba mwakomu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo amuna a Efraimu analalikidwa, napita kumpoto; nati kwa Yefita, Wapitiriraoji kuthira nkhondo ana a Amoni, osatiitana ife timuke nawe? Tidzakutenthera nyumba yako ndimotopamtupako.