Judges 12:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo nditaona kuti simunkafuna kundipulumutsa, ndidangochita utotomoyo nkuwoloka Yordani kukalimbana nawo Aamoni. Chauta adatithandiza kuŵagonjetsa. Chifukwa chiyani tsono mwabwera kwa ine lero lino kuti mudzachite nane nkhondo?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pakuona ine kuti simundipulumutsa, ndinataya moyo wanga ndi kupita kwa ana a Amoni; ndipo Yehova anawapereka m'dzanja langa; mwakwereranji tsono lero lino kundichitira nkhondo?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nditaona kuti simundithandiza, ndinayika moyo wanga pa chiswe ndipo ndinawoloka kukachita nkhondo ndi a Aamoni. Yehova anandithandiza ndipo ndinawagonjetsa. Nanga nʼchifukwa chiyani mwabwera kwa ine lero kuti muchite nane nkhondo?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pakuona ine kuti simunandipulumutsa, ndinataya moyo wanga ndi kupita kwa ana a Amoni; ndipo Yehova anawapereka m'dzanja langa; mwakwereranji tsono lero lino kundicitira nkhondo?