Judges 12:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Yefita adasonkhanitsa anthu onse a ku Giliyadi namenyana nkhondo ndi Aefuremu. Ndipo Agiliyadi adagonjetsa Aefuremu chifukwa chakuti Aefuremuwo ankati, “Inu Agiliyadi ndinu othaŵa ku Efuremu, ochokera pakati pa Aefuremu ndi Amanase.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Yefita anamemeza amuna onse a m'Giliyadi nalimbana naye Efuremu; ndipo amuna a Giliyadi anakantha Efuremu, chifukwa adati, Inu Agiliyadi ndinu akuthawa Efuremu, pakati pa Efuremu ndi pakati pa Manase.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Yefita anasonkhanitsa anthu a ku Giliyadi ndi kuchita nkhondo ndi Aefereimu. Ndipo Agiliyadi anagonjetsa Aefereimu chifukwa Aefereimuwo amati, “Inu a Giliyadi ndinu othawa kuchokera ku Efereimu ndi pakati pa Amanase.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Yefita anamemeza amuna onse a m'Gileadi nalimbana naye Efraimu; ndipo amuna a Gileadi anakantha Efraimu, cifukwa adati, Inu Agileadi ndinu akuthawa Efraimu, pakati pa Efraimu ndi pakati pa Manase.