Judges 12:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo Agiliyadi adalanda Aefuremu madooko a mtsinje wa Yordani. Pamene aliyense wothaŵa ku Efuremu ankati, “Ndiloleni ndiwoloke,” Agiliyadi ankamufunsa kuti, “Kodi ndiwe Mwefuremu?” Iye akayankha kuti, “Ai”,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Agiliyadi anatsekereza madooko a Yordani a Efuremu; ndipo kunatero kuti, akati othawa a Efuremu, Ndioloke, amuna a Giliyadi anati kwa Iye, Ndiwe Mwefuremu kodi? Akati, Iai;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Agiliyadi analanda Aefereimu madooko a mtsinje wa Yorodani. Munthu aliyense wothawa ku Efereimu amati akanena kuti, “Ndiloleni ndiwoloke,” Agaliyadi ankafunsa kuti, “Kodi ndiwe mu Efurati?” Ngati iye ayankha kuti, “Ayi”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Agileadi anatsekereza madooko a Yordano a Efraimu; ndipo kunatero kuti, akati othawa a Efraimu, Ndioloke, amuna a Gileadi anati kwa iye, Ndiwe M-efraimu kodi? Akati, Iai;