Judges 12:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iyeyu anali ndi ana aamuna makumi atatu ndiponso ana aakazi makumi atatu. Adakwatitsa ana aakazi makumi atatuwo kwa anthu osakhala a fuko lake, ndipo adakatengera ana ake aamuna aja ana aakazi makumi atatu a fuko lachilendo. Ibizaniyo anali mtsogoleri wa Aisraele zaka zisanu ndi ziŵiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anali nao ana amuna makumi atatu; ndi ana akazi makumi atatu anawakwatitsa kwina, natengera ana ake amuna ana akazi makumi atatu ochokera kwina. Ndipo anaweruza Israele zaka zisanu ndi ziwiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anali ndi ana aamuna makumi atatu ndi ana aakazi makumi atatu. Anakwatitsa ana ake akaziwo kwa anthu a fuko lina, ndipo ana ake aamuna aja anawabweretsera atsikana makumi atatu kuti awakwatire amenenso anali a fuko lina. Ibizani anatsogolera Israeli kwa zaka zisanu ndi ziwiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anali nao ana amuna makumi atatu; ndi ana akazi makumi atatu anawakwatitsa kwina, natengera ana ace amuna ana akazi makumi atatu ocokera kwina. Ndipo anaweruza Israyeli zaka zisanu ndi ziwiri.